Piksy - Uatchauya [Piksy & Hyphen] (Prod. Famous & Foxxy)
Name of album : Uatchauya Genre :Hip Hop
Thumbnail

Click here to download this song >> Desktop | Mobile


UATCHAUYA LYRICS
PIKSY x HYPHEN

INTRO (PIKSY)
Mesa unkati ndine ndekha
Mtima wanga sudzasweka
Mesa unkati ndine ndekha
Mtima wauchekacheka

CHORUS
Kukukonda ndakhaula
Kamtsinje kanga kauma
Wandiothetsa mbaula
Oh my oh my Uatchauya
Kukukonda ndakhaula
Kamtsinje kanga kauma
Wandiothetsa mbaula
Oh my oh my Uatchauya

VERSE ONE (PIKSY)
Mesa unkati ndine ndekha
Mtima wanga sudzasweka
Mesa unkati ndine ndekha
Mtima wauchekacheka
Eeh
Wandimeta mpala
Wandidyetsa mpunga wa miyala
Wandigulula mano
Wachiphwasula chipangano
Wandipatsa theche ngati moni
Wandipatsa usiku ngati morning
Wandikwera pa mutu ngati Drone
Wandilakwira opanda sorry

CHORUS
Kukukonda ndakhaula
Kamtsinje kanga kauma
Wandiothetsa mbaula
Oh my oh my Uatchauya
Kukukonda ndakhaula
Kamtsinje kanga kauma
Wandiothetsa mbaula
Oh my oh my Uatchauya

VERSE TWO (HYPHEN)
Maonekedwe ndi ngelo
Pakamwa nde pa munthu wa ndale
Kamunthu kodzadza ndi chinyengo
Zitheka bwanji mu tea kuthiramo Achale
Kundipatsa madzi momwera ziweto
Ndachezera kuothera nyale
Shaa
Wandigwiritsa wire wa EGENCO
Chiletso, kususa pansi utachotsa mbale
Wandiphwetsa chidale
Ka mtima kanga kukaika apo
Kutengana ndi anzako, busy kusewera chandamale
Iwe si munthu wamba
Ngati unafika poyimeta nkhanga
Olo maula ikunana
Iwe nde umadziwa kulanga
Ambiri akukamba

PIKSY
Wandiotchera msika
Wandilanda cha mzika
Wandibwiritsa Paprika
Nsima yanga waviika ah

BRIDGE (PIKSY & HYPHEN)
Mesa unkati ndine ndekha
Mtima wanga sudzasweka
Mesa unkati ndine ndekha
Mtima wauchekacheka

CHORUS
Kukukonda ndakhaula
Kamtsinje kanga kauma
Wandiothetsa mbaula
Oh my oh my Uatchauya
Kukukonda ndakhaula
Kamtsinje kanga kauma
Wandiothetsa mbaula
Oh my oh my Uatchauya