Robert Chiwamba - Mayi Anga Anali Mphunzitsi
Name of album : Mayi Anga Anali Mphunzitsi Genre :Spoken Word
Thumbnail

Click here to download this song >> Desktop | Mobile


Ndinaleledwa ndi mphuzitsi
Kubadwa kukula mpaka kumaliza sukulu
Sitinakhale ndi nthawi zachimwemwe zochuluka
Koma Mulungu anali yathu mbali
Mayi anga anali mphuzitsi

Tsiku ntsiku ankakhala pansi
Kulemba ma scheme ndi ma lesson plan
Chuma chawo chachikulu chinali njinga
Kupalasa mitunda yaitali tsiku ntsiku
Ntchito yomwe ngati dziko tinasankha kuyiyang'anira pansi
Koma sanaleme mayi
Chaka nchaka kutumiza ana ku ma secondary odziwika
Akakhale mabwana omwe adzapitilize kunyoza aphunzitsi
Kuwatukwana ngati palibe chomwe amadziwa
Kuwapondereza kuwatukwana nkuwayankhula zachabe
Mayi anga anali mphuzitsi

Akawerengera ngongole zawo pena ankalira mayi
Ana asanu ndi mmodzi adyanji malipiro osakwanira
Ntchito yopanda ma workshop zaka mpaka makumi awiri osakwezedwa olo
Yehova nde m'busa wathu sitizasowa ndiye inali yathu nyimbo tsiku ntsiku
Lero tadya mawa nlachauta ndiye unali moyo wathu
Mayi anga anali mphuzitsi

Nyumba zathu zambiri zinkakhala za pa sukulu zomwe ankaphunzitsapo mayi
Nyumba zodontha, zitseko zosakiyika zosamilitsira mipando mayi
Mipandoyo kukhala nayo ankakhala katapila mayi
Koma tsiku ntsiku tinkawaona ndi zochonga zambiri akuchonga mayi
Ndithu pokonza tsogolo la chigulu sankanyinyirika mayi
Chikakhale mmaofesi aulemelero chigulu
Kuti mapeto ake chidzawatukwane bwino mayi

Kuvala zovala zanyuwani ngati ana amphuzitsi pankakhala pa khirisimasi basi
Nsapato za pulasitiki pena makabudula ong'ambika
Chanzeru ku secondary popita tinkatenga chili chokazinga chimanga
Pena musakazinge chambiritu baba tingalowe munjala akuchondelera mayi
Koma chaka nchaka akusema tsogolo la aanthu amene adzakhale mabwana nadzakhale opanda nawo ntchito aphunzitsi mayi
Mayi anga anali mphuzitsi

Nde mayi ndi malipiro awo ochepa ankakwanitsa kutigoneka pa nkeka basi
Blangete loperepeseka kumafunda ana awiri awiri
Olo ndalama ya pillow sankakwanitsa
Mbale za pulasitiki zina zowotchedwa ndi moto wankhuni
Madzi kotunga kunkangokhala ku mjigo,
Magetsi sitinawadziwe
Palibe chuma ndingazakusiyireni ankatiyankhula misonzi ili mmaso
Chuma ndingakupatseni ndi maphunziro omwewa
Pamene nduphunzitsa ena nanu phunzirani
Mudzakhale pabwino nimuzadyelere
Kwa ine kwatha ngati mphuzitsi
Nzakondwera ti makatapira ndutengati titakupindulirani
Njinga yakapalasa ndimapalasa itakubalirani magalimoto
Koma kuti moyo wathu aphunzitsi nkuzasintha nzokaikitsa
Mphatso yanga ana anga ndi maphunzirowa
Ndi kusaiwala Mulungu ndinso Kudzichepetsa

Lero mayi anapuma
Mphavu zinapita njinga sangapalase
Pension yawo kuyiona mutha kulira
Moyo wa iwo ndaphunzitsi anzawo omvetsa chisoni
Mu ukalamba wawo alibe medical scheme
Zinthu zinadhula pension sikwana
Nthaka inaguga koma feteleza pawokha sangakwanitse
Chipumileni mayi zambiri zasintha
Maboma abwera nkupita
Koma mnyozo kwa aphunzitsi sunathe
Ulemu kwa maphunziro sitinayambebe kupereka
Otonzedwa, otukwanidwa, oyang'aniridwa pansi ndi mphuzitsi
Zamisonzi yawo sizimveka
Mapempho awo ndi phwete kwa odzitcha okha ozindikira
Kudeleredwa ndi ana ndi asukulu komiti kosayamba
Salary, pension zachisoni
Ntchito zopanda allowance

Nkamaona izi misonzi imatsika
Chifukwa nzomwe ndakula nazo
Ndipo simungandinamize kalikonse ka mphuzitsi anta
Nkofunika tikanasintha
Kupereka ulemu kwa onga anga mayi aphunzitsi
Kutenga maphunziro ngati chofunika kuposa zonse
Bajeti maphunziro kumalandira kuposera kalikonse
Osayiwala palibe zaumoyo, zaulimi, zachilichonse zopambana opanda maphunziro
Koma mwina mwa nthawi zonse ndakatuloyinso simukhala nayo attend
Poti ikukamba za ulemu kwa mphuzitsi
Koma kwa tonse amene takulira mnyumba mwa mphuzitsi
Sitingayankhule mtudzu olo pang'ono
Ma Pempho awo olo atakhala osatheka mu nthawiyo
Sitingawayankhule mobwafula
Anthuwa akumana nazo ndipo amakumana nazo zokhoma
Osaiwala sindikungoyankhula
Mayi anga anali mphuzitsi