Pure Days - Cholinga (Prod. Khumbo Kaliwo)
Name of album : Cholinga Genre :Gospel
Thumbnail

Click here to download this song >> Desktop | Mobile

C H O L I N G A

Verse 1
Akandiona ndili chonchi, Mumtima mwake sava bwino, Amangofuna mdzingolira, Chimwemwe tsaya kusekerera, wandipheraana anga,Chuma changa wandilanda Matenda mmoyo mwanga Thupi loseli ndizilonda Cholinga chake ndimudziwa Akufuna mtukwane Mulengi, Koma monga Yobu mkakamira Choka satana kumbali yanga Yemwe ndimampembedza ndimamdziwa Ndiye Mulungu wamakamu Olenga kumwamba mdziko Ndipo ndikakamira padzina lake
Chorus*2
Ndicho cholinga cha mtima wanga N d i k a l o w e m o m’m w a m b a Ndicho cholinga cha mtimamu N d i k a l o w e m o Ine Mchikondwerero cha mwana wa Mulungu N d i k a l o w e m o m’m w a m b a Kuli ambuye mkakhaleko N d i k a f i k e k o

Verse 2 Palibe china mdzikoli Chimandipatsa mtendere,Kuposa kupezekamo Munyumba yake ya Yehova, Palibe china mdzikoli Chobweretsa chimwemwe mtima mwanga Kuposa uthenga wabwino, Kuulalika kudziko lonse, Ine ndanyamula mtanda wanga Ndimayenda ndi ambuye Ndidzatumikira khristu Kulikonse andituma Kaya akuti mkalalike Kaya akut mkadzudzule,Ndikatonthoze olira Kudziko loseli mkafika Ndilibe mantha mmoyomu ndidzanyozedwa naye khristu Ngakhale kumanda kumene Ndili nganganga pa ambuye

Chorus*2
Ndicho cholinga cha mtima wanga N d i k a l o w e m o m’m w a m b a Ndicho cholinga cha mtimamu N d i k a l o w e m o Ine Mchikondwerero cha mwana wa Mulungu N d i k a l o w e m o m’m w a m b a Kuli ambuye mkakhaleko N d i k a f i k e k o

Composed By:Pure-days