1853Downloads
Faith Tsoka - Chikondi
Click here to download this song >> Desktop | Mobile
Verse 1
Mukandiwona ine ndilinkulakwitsa
(If you see me in error)
Mundikonze mwa chikondi
(Correct me with love)
Kusiyana ndikuti mukawuze wina
(Instead of going to tell someone else)
Mundiphela chikoka changa
(You will kill my influence)
Tikamuwona mbale, mlongo, alinkulakwitsa
(If we see a brother, sister, in error)
Timukonze mwa chikondi
(Let’s correct them with love)
Kusiyana ndikuti tikawuze wina
(Instead of going to tell someone else)
Timuphela chikoka chake
(We will kill their influence)
Chorus 1
Chikondi; chikondi chimapilila
(Love; love is patient)
Chikondi; chikondi chilibe nsanje
(Love; love does not envy)
Chikondi; chikondi ndi chokonza
(Love; love is corrective)
Chikondi; chikondi ndiye Mulungu
(Love; love is God)
Chikwilila unyinji wauchimo
(It covers a multitude of sins)
Verse 2
Pali abale (alongo) ena akaona choipa
(There are some brother (sisters) when they notice an error)
Pa mbale (mlongo) nzawo samakamukonza
(On their brother (sister), they don’t correct them)
Amapita nakawuza abale (alongo) ena
(They go and tell other brothers (sisters))
Umenewo ndi mzimu wamiseche
(That is a gossiping spirit)
Chorus 2
Miseche; miseche idzetsa udani
(Gossiping; gossiping brings enmity)
Miseche; miseche idzetsa migawano
(Gossiping; gossiping brings division)
Miseche; miseche idzetsa mikangano
(Gossiping; gossiping brings arguments)
Miseche; miseche ichokela kwa Satana
(Gossiping; gossiping comes from Satan)
Tisayanjane nayo miseche
(Let’s not gossip)
Verse 3
Pali abale (alongo) ena safuna kuvomela
(There are some brothers (sisters) that don’t accept)
Kukozendwa akalakwitsa
(Correction when they are in error)
Amakwiya kapenanso amanyanyala
(They get angry or upset)
Umenewo si mzimu wa Mulungu
(That’s not God’s Spirit)
Chorus 3
Mzimu woyela; Mzimu woyela ndiwololela
(The Holy Spirit; the Holy Spirit is yielding)
Mzimu woyela; Mzimu woyela ndi wa mtendere
(The Holy Spirit; the Holy Spirit is peaceful)
Mzimu woyela; Mzimu woyela ndi ofatsa
(The Holy Spirit; the Holy Spirit is meek)
Mzimuwo; Mzimu woyela ndiye Mulungu
(The Holy Spirit; the Holy Spirit is God)
Kukhala moyo mkati mwa ife
(Living a life inside of us)
Ending
Chikondi; chikondi ndichokoma mtima
(Love; love is kind)
Chikondi sichimadzitama
(Love does not boast)
Chikondi sichimapsya mtima
(Love is not easily provoked)
Chikondi chikondwela ndi choona
(Love rejoices in the truth)
Chikondi chiphimba machimo onse
(Love covers a multitude of sins)
Chikondi sichitha nthawi zonse
(Love does not end)