20596Downloads
Phyzix - Chitsanzo ft Danny Kalima (Prod by Dare Devilz and BFB)
Click here to download this song >> Desktop | Mobile
Yeah
Iwe ndi uti?
Gamba wopemphera/ C'mon!
Yeah, Phyzix
Danny Kalima
-Hook-
Ngati ndaborna winawake aborna
Ngati ndasintha winawake asintha
Ngati ndamudziwa Yesu/ amudziwa Yesu
Amandiwelenga ngati ndine bukhu
Mafanawa/ Mayuthiwa
Ndikhale ndikhale
Chitsanzo cha bho
Cha mafanawa/ Cha mayuthiwa
Ndikhale ndikhale
Chitsanzo cha bho!
- Verse 1 - (Phyzix)
Amandidziwa/ Nsanje to Chitipa
Nyimbo ya Cholapitsa inanditchukitsa
Tsa/ Tsa/ Tsa/ Ine ndine Phyzo
Sikuti ndisintha dzina poti ndinaborna
Ndimadziwa ntchito zanga ndi zonyasa
Ndine munthu wolephela ndine wochimwa
Grace/ Grace// chisomo cha Ambuye
Ndichomwe ndikufuna kuti mwina ndingalimbe
Ndichilitseni/ Ambuye dalitseni
Muwapatse moyo wautali Amayi/ Masten
Dziko/ ndi lovuta
Moyo/ ndi wozunza
Timafuna winawake a role model
woti zake zikuyenda/ akuwina nkhondo
Si Yudasi/ si Jemusi/ si Phyzix
Ndi Yesu basi
-Hook-
Ngati ndaborna winawake aborna
Ngati ndasintha winawake asintha
Ngati ndamudziwa Yesu/ amudziwa Yesu
Amandiwelenga ngati ndine bukhu
Mafanawa/ Mayuthiwa
Ndikhale ndikhale
Chitsanzo cha bho
Cha mafanawa/ Cha mayuthiwa
Ndikhale ndikhale
Chitsanzo cha bho!
- Verse 2 - (Phyzix)
The Real Elements/ Q/ Marvel
Plan B/ Stix/ anandipatsa chitsanzo
Kuti Hip Hop idzimveka ngati Nyambo
Akupitilizabe kundipatsa chitsanzo
Anakula Anaborna Anakwatila
Ndinakula Ndinaborna Ndikukwatila
Mbali yanga ngati M'khristu ndipange
Dziko sadzaliwononga ndi madzi
Moto kuupewa ndikulapa tchimo
Kumapemphera kumawelenga baibulo
Kumasonkhana ndi anthu/ Mpingo
Mundipatse mtima wodzichepetsa
Mzimu woyera tchimo muzindiletsa
Kutchuka kwanga kuzilemekeza inu
Chuma changa chakhumi kupatsa inu
Ndidzikonda momwe mukondera inu
-Hook-
Ngati ndaborna winawake aborna
Ngati ndasintha winawake asintha
Ngati ndamudziwa Yesu/ amudziwa Yesu
Amandiwelenga ngati ndine bukhu
Mafanawa/ Mayuthiwa
Ndikhale ndikhale
Chitsanzo cha bho
Cha mafanawa/ Cha mayuthiwa
Ndikhale ndikhale
Chitsanzo cha bho!
- Verse 3 - (Danny Kalima)
Amayi anati/ opanda Yesu sungakwanitse
Amayi anati/ ugwiritsitse Yesuyo
Lero ndakonzeka kusintha moyo wanga
Munayamba kale kundiyitanaaaaa!
- Verse 4 - (Phyzix)
Mulungu wanga ndabwera pamaso panu
Mundikhululukire zochimwa zanga
Ambiri zawasocheletsa nyimbo zanga
Ndikupepesa/ Ndikupepesa
Ngati mungakhululuke/ Ndapepesa
Ndikufuna mwana wanu/ Yesuyo
Ali mkono wakumanjayo/ Yes uyo
Sindidzamukana olo ngati Petulo
-Hook-
Ngati ndaborna winawake aborna
Ngati ndasintha winawake asintha
Ngati ndamudziwa Yesu/ amudziwa Yesu
Amandiwelenga ngati ndine bukhu
Mafanawa/ Mayuthiwa
Ndikhale ndikhale
Chitsanzo cha bho
Cha mafanawa/ Cha mayuthiwa
Ndikhale ndikhale
Chitsanzo cha bho!
-Hook-
Ngati ndaborna winawake aborna
Ngati ndasintha winawake asintha
Ngati ndamudziwa Yesu/ amudziwa Yesu
Amandiwelenga ngati ndine bukhu
Mafanawa/ Mayuthiwa
Ndikhale ndikhale
Chitsanzo cha bho
Cha mafanawa/ Cha mayuthiwa
Ndikhale ndikhale
Chitsanzo cha bho!
-Outro-
Thank you Jesus
Forgive me all of my sins
I make you my Lord and Saviour
Amen.
J.E.S.U.S
Jesus!