Hala Music - Duduluza feat. Methuselah, Mista Gray & Maya
Name of album : Duduluza Genre :Gospel
Thumbnail

Click here to download this song >> Desktop | Mobile


Intro:

Eyooo!! Mfundo za Mingoli, Pali zambirimbiri zotibwezera mbuyo, pali Nkhondo zoti timenye

(Zilipo zambiri) yea!! Nde Tangomva Izizi...! Nkhaza m'mationetsera (Sitingasiye kulalika),

kuphinjika kulikonse.. Kulibe mphanvu yogwetsa chomwe chili cha Uzimu (Ndizosatheka),

HALA MUSIC, PLAN_A Eyoo!! Tangomvani Izizi!! Yheaa Methu-Music.

VERSE 1: METHUSELAH

Ndisanaike ndemanga kaye, imani ndiyambe ndamanga kaye// ulendo wanga ndiwopanda corner

ndiwakumwamba sindigwa mphwayi// ndanyamula Yesu mthupi mwanga mtanda ndi katundu

nduyu ndamangayu// mwamwayi mwazisomo ngati pwayi!! system ya thupi ndiiyi ndaphayi!!!

Ndachita chosita khwimbi ndi simbi ndati ndisimbe zamaSouls// ndalimbana nako inde

kwabwino ine chiphona cho Borner ndi cha Muscles//ngati Dobadoba wa ku malawi, ndili ndi

ncheni ndikufuna tchana//Methu ndi umphawi sizimatchana siku Jon kokha komwe kuli tchana

(Khuli Tchana)

Ndikubwera ndi gulu langa lonse HALA MUSIC ndikuvunga mivi// Ndatseka mapirikaniro anga

ndatsegula mtima kuti // Ndisazembe ngati yonah ku ninive ndiwenge tchimo ngati sponge pa

zikakanga// Musalore dziko lindikore ndisalalikile zithu zoti sizanga!!

Dziko limafuna tiziyimba kulalika zithu zolibebera// Tikanena kuti Yesu ndi mulungu mtima

mwawo timakhala opepera// timatchedwa makape, agwape anthu opepera ofera za ena//

kwaiwowo ndife chifukwa mulungu analengera Jahena

HOOK: MAYA

Yeaaaa Zingavute zingatani, anthu anganene Chani, sindingasiye kumpembedza Wanga

mulungu wamakamu.

Zingavute zingatani, anthu anganene Chani, sindikatope kumuimbila Wanga mulungu

wamakamu.

Andijeda, andinena, andinyoza (DUDULUZA)!!!

Andipekela zinkhani zamabodza (DUDULUZA)!!!

Andiseka, andithoka, andiswaya (DUDULUZA)!!!

Anditenga opanda pake anditayaaa..!!!!

VERSE 2: MISTA GRAY

Zimatero makamaka zikakhala kuti penapake sizikufwamba//

Timijedo amayamba, kumakunena timiseche kumbali kukamba //

Akakalowa kumwamba ine ndikalowa kutuluka kulowa kutukula//

Akakapulumuka nde kuti padzikoli opulumuka ndiochuluka//

Ati born again wabodza, mwaiye mulibe kudzodza //

Akaphoza amakonza timaboza tokunyoza //

Zoipa kuzifotokoza ndizala kukuloza kukutonza //

Ati uone Gazi matatalazi, ma braz kuvikana mmazi//

Kulondana phazi basi fanzi ndi paparazzi//

Mayazi manyazi nkhani zazii kumponda nnasi pansi//

Kweni kweni nchani chikuchitikachi kachi (Zii)//

Taiwala zoti ndife wamulungu kachi kachi (Si)//

Tisapite kutali chilungamo nachi nachi //

(Si)fe oweluza Mulungu ndiye judge judge (huh)//

Mmalo motolana tikagwa, tayamba kutolana ma fault//

Tizuzulane mwachikondi Mulungu sanaike mumtima mwathumu court! Nde ine ine zingaa...

HOOK: MAYA

Yeaaaa Zingavute zingatani, anthu anganene Chani, sindingasiye kumpembedza Wanga

mulungu wamakamu.

Zingavute zingatani, anthu anganene Chani, sindikatope kumuimbila Wanga mulungu

wamakamu.

Andijeda, andinena, andinyoza (DUDULUZA)!!!

Andipekela zinkhani zamabodza (DUDULUZA)!!!

Andiseka, andithoka, andiswaya (DUDULUZA)!!!

Anditenga opanda pake anditayaaa..!!!!

VERSE 3:METHUSELAH

Tavungiridwa mikondo pakhondo talamitsidwapo ndizigogodo// nkhonya kuthetheka kuchoka

ngondya zonse kuthilidwa khoko ndizikokoto// kupereka moni kwa oimba otchuka mtima

mwake nkumati izi ndi ziti// Kuponderezedwa kuma show MC,Dj kunditcholera CD!!

Ndimaona zambirimbiri mu mbiri yanga yoimba ndikayamba komwe ndachokera// ndimaona

Tate,Mwana Mzimu oyera akundiuza kuti mchipululu simofera// Azanga amene ndinayamba

kumaza nawo zaka 8 zapitazo ndi awo kumanda apitawo// Kufika Lero sizamwayi ndichisomo

sizophweka kukhala kapitawo!!

Miyoyo yambiri ikusochera ndi lucifer wothothoka mapiko// kufera mayina achipembedzo ali

ma bungwe otchedwa mipingo// kupanda kumanga nyumba Jehovah omanga amanga pa oipa

maziko//Chipulumutso chili mwa Yeshuah Messiah palibeso kwina Padziko!!

HOOK: MAYA

Yeaaaa Zingavute zingatani, anthu anganene Chani, sindingasiye kumpembedza Wanga

mulungu wamakamu.

Zingavute zingatani, anthu anganene Chani, sindikatope kumuimbila Wanga mulungu

wamakamu.

Andijeda, andinena, andinyoza (DUDULUZA)!!!

Andipekela zinkhani zamabodza (DUDULUZA)!!!

Andiseka, andithoka, andiswaya (DUDULUZA)!!!

Anditenga opanda pake anditayaaa..!!!!

End