Faith Mussa - Selofoni ft Foxxy
Name of album : Selofoni (Single) Genre :Gospel
Thumbnail

Click here to download this song >> Desktop | Mobile


Chorus
Akhristu ambiri lero amapembedza Selofoni
Akhristu ambiri, Mulungu wao ndi Selofoni

VERSE 1
Akakhala pa nyumba, amakhalira pa selofoni
Samacheza ndi ana, tsiku Lonse pa selofoni
Akakumana ndi vuto,mmalo moti apemphere,
Amakalemba pa fesibuku, Mulungu wao ndi Selofoni

Kaya akupalasa njinga, nkono wina pa Selofoni
Akafika ku ntchito, amatenga Selofoni
Ayambe kumvera nyimbo, nyimbo zosalongosoka
Ndekuti tsiku lonse woye woye woye woye kuba nthawi ya ofesi ambuye

Chorus
Akhristu ambiri lero amapembedza Selofoni
Akhristu ambiri, Mulungu wao ndi Selofoni

VERSE 2
Popita ku chalichi, samaiwala Selofoni
Amalisiya Baibulo, koma osati Selofoni
Abusa akulalikira, iwo ali pa fesibuku
Uku akugwedeza mutu, koma sitili limodzi (Selula foni)

Leo machalichi akudzadza, koma omvetsera ndi ochepa
Anthu ambiri maganizo ali kutaaaaaaaaali

bridge
Zalowa chibwana,
chibwana cha mchombo lende
Zalowa chibwana,
Ngati inakufera pa mtanda
Zalowa chibwana,
Pa mtanda Selofoni
Zalowa chibwana,

VERSE 3
Kachinthu kofunikira, ukakagwiritsa ntchito bwino
Anthu akupeza mabanja, mbalume pa selofoni
Mabanja ena kutha kumene, nkhani yake ya Selofoni
Mautumiki akutha kubadwa, kutumikira pa selofoni

Isatidyere nthawi ya pemphero, isalande malo a Yehova
Tachezaniko ndi akazi wanu, lero lokha foni ipume
Isatidyere nthawi ya pemphero, isalande malo a Yehova
Inu tachezaniko ndi amuna anu, lero lokha foni ipume

OUTRO
Akhristu ambiri lero amapembedza Selofoni
Zalowa chibwana
Akhristu ambiri, Mulungu wao ndi Selofoni
Zalowa chibwana
FONI SELULA FONI!!!