
Click here to download this song >> Desktop | Mobile
Chorus x2
Chilichose chili ndi nthawi ndi Malo
Usalire mai Malawi ndi dalo
Kuti ugonjetse umphawi
Thukuta lako lidzagonjetsa njala
1st Verse
Ana wako udzawalera
Bwino lomwe udzawa phunzitsanso moyenela
Zamakhalidwe a muno m'mdera
Eh mtendere wako wamawa ine ndalosera
Udzanka ndi chimwemwe komwe udzalowera
Samala popeza salambula pofera
Kalikonse kowuluka kadzatera
Woipayo akumadana ndidzomera
Kufuna kuzula mbeu yomwe ndaokera
Usatsike, ukagwa dzuka ndipo kwera
Popeza ndiwe woyera
Chorus x2
Chilichose chili ndi nthawi ndi Malo
Usalire mai Malawi ndi dalo
Kuti ugonjetse umphawi
Thukuta lako lidzagonjetsa njala
2nd Verse
Sitidzatsata zikhalidwe zachilendo
Milungu yakufa tidagonjetsa m'Armagedo
Kufuula kufika konseko
Kuitana ana omwe ali kwa dziko mapeto
Ndati, Bwerani kunyumba
Ndife amodzi, ndife mbumba
A mai wako akukhumba
Atangokuona ndithu m'mwamba adzadumpha
Chorus x2
Refrain
Ana wako udzawalera
Bwino lomwe udzawa phunzitsanso moyenela
Zamakhalidwe a muno m'mdera
Eh mtendere wako wamawa ine ndalosera
Udzanka ndi chimwemwe komwe udzalowera
Samala popeza salambula pofera
Kalikonse kowuluka kadzatera
Woipayo akumadana ndidzomera
Kufuna kuzula mbeu yomwe ndaokera
Usatsike, ukagwa dzuka ndipo kwera
Popeza ndiwe woyera