Kelvin Sings - Mamuna Amene Ndili
Name of album : Mamuna Amene Ndili Genre :Afro Soul
Thumbnail

Click here to download this song >> Desktop | Mobile


Verse 1

Unandipeza ndili lova
Ndilibe kalikonse
Mmatumba mwanga mobooka
Nyumba yopanda khonde

Ndekuti dzuwa likaomba
Mkati khuma kumaonda
Iweyo utandiona
Sindimvetsa chomwe unakonda

Utabwela unandilimbikitsa
unati ndisabwelele m'mbuyo
Chomwe chinali chako naneso ndi changa
Kuti ndisamasowe tulo

Bridge

You must be a saint or something
How could you give it all
And ask for nothing in return

Pre chorus

Ndikusowa chonena ine
Malangizo ako
Andifikitsa pena ine
Poti ndiine wako

Hook
Bwela umunyadile mamuna amene ndili
Kamba ka iwe X2


Verse 2

For I was never enough
I had room for you in my life
Ndizizwa ndichisankho chako ooh
Chokhala nane ngakhale mnyumba mwanga
Mpando munalibe

Pomwe sizinkandiyendela
Unagwada ndikupemphela
Pamene mwayi unatetela
Unandiuza ndimukumbuke namalenga

Ndikamabwela ku ulenje
Mmalo mwa nyama ndi denje
Nkumandilandilabe ndi chimwemwe
Ine pakamwa kakasi

You know pena ndikati ndidye frus
Most of my days i am under the weather
But i believe God gave you to me
To help me keep it together

Bridge

You must be a saint or something
How could you give it all
And ask for nothing in return

Pre hook

Ndikusowa chonena ine
Malangizo ako
Andifikisa pena ine
Poti ndine wako

Hook

Bwela umunyandile mamuna amene ndili
Kamba ka iwee X4 ( chikondi ndachimvesesa// nkhawa zonse unathesa// chikondi ndachimvesesa I'm a better man// sindikanakwanitsa ndekha// i needed you to get me to where i am right now//)