Gwamba - Mapiko ft Kell Kay (Prod. BFB)
Name of album : Mapiko Genre :Gospel
Thumbnail

Click here to download this song >> Desktop | Mobile


VERSE 1 (GWAMBA)

Ambuye, akuti mudzabwera ngati mbala

Mudzapeza anthu ena atangokhala

Ena ali ku Bala (Bar)

Ena ali ku Vep

Ena akuthamanga kukaona nyau kwa Senti

Akuti musanabwere kudzabwera chi beast

Pa chipumi pake pazakhala zima six

Ndiye ndikumadzifunsa ndekha chenicheni nchiti?

Akumakambanso zambirimbiri scientist

Bible lanu anthu analipanga twist

Zosawasangalatsa anapanga delete

Mpingo uli onse ukuona ngati ukukhonza

Sakudziwa amadziwa zoona ndi Yehova

-

BRIDGE (GWAMBA)

Ndimadziwa Mbuye mudzabwera ndithu Yahweh

Kudzatijaja tonse ndipo palibe atadzathawe

Ndiye chonde mukadzabwera musadzandiiwale

Ndine munthu wochimwa kwambiri koma mudzandipatse

-

HOOK (Kell Kay)

Mapiko

Mudzandipatse mapiko

Mapiko

Mudzandipatse mapiko

Ndidzauluke nanu

Ulendo wa kumwamba

Mapiko

Mudzandipatse mapiko

-

VERSE 2 (GWAMBA)

Awa akuti ndi a Pastor

Anthu okumwa mowa sawasangalatsa

Pa dziko lapansi pompa ayamba kujaja

Ayiwala ntchito yomwe inu munawapatsa

Gospel yawo akuti amayimba okhaokha

Tikayimba ndi wa secular amayamba kuthoka

Akuti uyimba bwanji ndi mafana olowelera?

Koma mesa Mulungu amafuna nkhosa zosochera

Akujaja

Alowa mmalo mwanu Namalenga

Kuchotsa chisoso mmaso mwanga mwawo muli mchenga

Akuti ndi akhristu aakulu ife ndi tiana

Akujaja anthu ena poti amachimwa mosiyana

-

BRIDGE (GWAMBA)

Koma ndimadziwa kuti mudzabwera ndithu Yahweh

Mudzatijaja tonse ndipo palibe atadzathawe

Ndiye mukadzabwera chonde musadzandiiwale

Ndine munthu wochimwa kwambiri koma mudzandipatse

-

HOOK (Kell Kay)

Mapiko

Mudzandipatse mapiko

Mapiko

Mudzandipatse mapiko

Ndidzauluke nanu

Ulendo wa kumwamba

Mapiko

Mudzandipatse mapiko

-

(GWAMBA)

Nthawi zambiri ine ndikamapemphera

Mtima wanga umakhala uli kwina

Nkona Ambuye wanga ndikumalephera

Kusiya njira zanga zina za mumdima

Nthawi zambiri ine ndikamapemphera

Mtima wanga Ambuye umakhala uli kwina

Nkona pano ine ndikumalephera

Kusiya njira zanga zina za mumdima

Ndiye mudzandipatse

-

HOOK

Mapiko

Mudzandipatse mapiko

Mapiko

Mudzandipatse mapiko

Ndidzauluke nanu

Ulendo wa kumwamba

Mapiko

Mudzandipatse mapiko