Evanz Muzik - Dear Mahopu pt4
Name of album : Dear Mahopu Genre :Hip Hop
Thumbnail

Click here to download this song >> Desktop | Mobile


Dear Mahopu IV Lyrics.

...Masiku ano n'nasiya kuzitengera.
Sindikakamira ngini ndikayilephera.
Sindithokesana ndi chick yomwe simandifila.
Kapena yoti, ingofuna tizingotchila.

Man zaka folo, ndithu zaka folo.
Nthawi zonse nkavayila angondiombetsa pholo.
Mahopu ake omwe aja akale kale aja.
Pompano zimamveka agwidwa ndi man aja.
Nthawi zonse nkavayila angondiombetsa pholo.
Mahopu ake omwe aja akale kale aja.
Pompano zimamveka agwidwa ndi man aja.

Ndalemba zibaluwa zingapo zokamupeza.
Ndikati ndimamufila amayesa ndingocheza.
Day one n'nakumana naye nditageza.
Nditavala descent ndikuchokera kopraiser.

Sin'nampaseso moni, ndidangomuyang'ana ndikungoyamba ndi funso,"kodi ulibe chisoni?
Sumakhala sure mpaka pano zaka folo
Kuyambira 2012 ndakhala Wako kapolo.

Kuwerengetsa anthu zomwe ndimakulembera.
Kundisandutsa kape poti ndimawerengera.
Fans imandiseka, Ku geli ndimaphweka.
Ena amayesa makalata aja ndiongopeka.

Kodi ndiwe otani? Unagwidwa ndi ndani?
Lero undiyankhe face to face osasintha nkhani.
Kwathu sindikudya ngati ndamanga ramadhan.
Mwina ndimufunse X Wako anapanga chani.

Ndikulephera kugwira wina
Kudikira you
Poti zaka zonsezi mahope anga ndi you
Kundikana ndi za bhobho.
Bola osalola wina
Bola nkhani ndisakayimvere kwina.

Mahope anali phee
Kankhope kamanyazi.
Nane thupi litauma zoti ndithawe mayazi.
Nkaziyu wandizuza heavy kwa zaka zingapo
Zoti ndingangomusiyasiya ndi zovutirapo..

Anandiyankha mwachifatse ngati namwino.
Ndipo chichewa chake chomveka bwino bwino.
Sanadzikolekole, pena kulowa nkhani za personal olo kunenako sorry...

"...Koma akazi onsewa nawe?
Nsakuitane mahopu eh eh ndisaseke nawe?
Basi poti ndimacheza nawe?
I just take you as a friend and I'm surprised you think about me that way.

Eh kunditchukisa basi ndi nkhani izizi?.
Anthu akamva aziti ndimakupanga tease?.
Koma sindingangolora who am I tryna please?.
Izi ndi nkhani zovuta wekha you know how it is.

Kugwidwa ndi iweyo anthu aziti wagwera.
Aziti mwina ndinakulora nditaledzera.
Ndili ndi anzanga ena abho ndikupezera.
Ma pics ndi ma number awo ndikutumizira.

Nkhani za zibwenzi pano nzongopusisana.
Nkhondo ya chinsinsi yothera kuphulisana.
Ma scandal ausilu mpaka kutchukisana,
Kumenyana cuz of jealous mpaka kutupisana.

Ofcoz Ndimakufila koma iweyo ndiwovuta.
Apapaso mwina wabweranso utakhuta.
Ndinava umasuta, ganja,
Anzanga adakuona uli ku camp ya pa ground la manja.

Ndipo zosakukhala tona ukuda zala.
Kukubweraku basi man musiye kundihala.
Kugwidwa ndi iweyo anthu aziti ndapala.
Munthu okonda chamba every friday ku Bara."

Ehem...ukulakwisa ukusokoneza nkhani.
Olo ndifotokoze uzipangabe makani.
kodi chinalakwika pa ineyo ndi chani?
Chomwe chimapangitsa ndisakhale Wako man?.

Sikoyamba kundinena zambiri ndimangonvera.
Nkhani zake zabodza zosowa komwe zachokera.
Ndimakufunitsitsa nchifukwa ndimangobwera.
Koma sikuti ndipuse chifukwa ndimakufela.

Ndimakuhopera koma umandiphwekesa.
Ndimapepera daily nkamakuchaser
Ndikufuna undiuze chomwe chimakuletsa.
Lero ndilomaliza nkhaniyi sinzabwereza.

Ndinaona ti misonzi mu maso amahopu
Ine kumangothoka zi mbalume non stop.
Mfundo zinkangobwera ngati pali likasa.
Ndinkamuthira wise ndipo zinkandiwaza.

Tinayamba kuyenda, kumperekeza kwao.
Ma babe ena kundiona ndimangoti zawo.
Tinkayenda shosholo yoti sitinayendepo.
Sindinavale top koma sindimanva mphepo.

Tikusiyana ndinadabwa anandihaga.
Ine ndati ahh pompanopa andikankha.
Ine kudabwa mpaka 2 minutes yonse yatha.
Atangondimatirira ndithu ngati nthata.

Ndinabalalika, eh zinali crazy.
Mtima kugunda confidence sindinayipeze.
Ngati ndi filimu yafika Kumathero.
Nkumadabwanso kodi kani moyo umatero.

Zosatheka zimatheka.
Swazi amagwira,
Mkazi ovuta uja si uyu wanditsamira.
Nzoona chikondi sichipezekeza Ku shopu.
After zaka folo ndagwira Dear Mahopu...