Cassim Ibrahim - Zimawapweteka
Name of album : Zimawapweteka Genre :Afrobeat
Thumbnail

Click here to download this song >> Desktop | Mobile


INTRO

Hash!
Strongingo...

*CHORUS*

Zimawapwetekaaaa!
Zimawawawaaaa!
Amapsa mtimaaa!
Asovengeee!

*VERSE 1*

Amayipitsa mbiri yanga/
Sandifunira zabwino mu moyo wanga/
Zikamayenda zinthu pa banja langa/
Sagona nane tulo!

Atchera misampha mu njira yanga/
Koma ndiyenda ndi mdidi ndi Yesu wanga/
Ayesetsa kuwononga tsogolo langa/
Koma Yesu sanalole!

Ankati sindikwatiwa ine!
Ankati ndidzafa mbeta ine!!
Lero ndapeza banja!
Zikuwapweteka...!

Ankandipondereza ine!
Ankandiwonera pansi ine!
Lero Chauta wandikweza ine!
Zikuwapweteka!

*(Back to Chorus)*

*VERSE 2*

Adani kuyesa kutembelera/
Kuti zinthu zisiye kukuyendera/
Koma Mulungu madalitso angowonjezera/
Adani akowo sakumvetsetsa...

Akakuona kusekelera (kumwetulira)/
Koma kumbali malupanga akusula/
Kuchalira moyo wako kuthusula/
Koma nkhondo Yehova akumenyera...

Angokhalira kukunyoza iwe/
Cholinga ubwelere m'mbuyo iwe/
Angofuna akugwetse iwe/
Ukakamire Yesu...

Ati ndiwe wa matama iwe/
Ati athana nawe iwe/
Ndithu akukuopseza iwe/
Iwe kakamira Yesu...

_*(Back to chorus)*_

*BRIDGE*

Chisomo chili mbwe mbwe mbwe!
Cha Yehova chili mbwe mbwe mbwe!
Madalitso ali mbwe mbwe mbwe!
Chitetezo chili mbwe mbwe! X2